-
Yeremiya 37:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndiyeno asilikali a Farao anabwera kuchokera ku Iguputo+ ndipo Akasidi amene anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu atamva zimenezi anachoka ku Yerusalemu.+ 6 Kenako Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti: 7 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Mfumu ya Yuda imene yakutumani kudzafunsira kwa ine mukaiuze kuti: “Taonani! Asilikali a Farao amene akubwera kudzakuthandizani adzabwerera kwawo ku Iguputo.+
-