9 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu,
Iwe dzanja la Yehova!+
Dzuka ngati masiku akale, ngati mʼmibadwo yakale.
Kodi si iwe amene unaphwanyaphwanya Rahabi,+
Amene unabaya chilombo chamʼnyanja?+
10 Kodi si iwe amene unaumitsa nyanja, amene unaumitsa madzi akuya kwambiri?+
Si iwe kodi amene unapangitsa kuti pansi pa nyanja pakhale njira yoti anthu owomboledwa awolokerepo?+