7 “Ndinakusiya kwa kanthawi kochepa,
Koma ndidzakusonkhanitsa pamodzi mwachifundo chachikulu.+
8 Chifukwa cha mkwiyo wanga waukulu ndinakubisira nkhope yanga kwa kanthawi,+
Koma chifukwa cha chikondi changa chokhulupirika chimene sichidzatha ndidzakuchitira chifundo,”+ akutero Yehova, Wokuwombola.+