-
Genesis 32:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Pomaliza, Yakobo anatsala yekhayekha. Kenako munthu winawake anayamba kulimbana naye mpaka mʼbandakucha.+ 25 Munthuyo ataona kuti Yakobo sakugonja, anamugwira pamalo amene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno ndipo polumikizanapo panaguluka mmene ankalimbana naye.+ 26 Atatero anauza Yakobo kuti: “Ndisiye ndizipita, chifukwa kukucha tsopano.” Koma Yakobo anayankha kuti: “Sindikusiya mpaka utandidalitsa.”+
-