-
Deuteronomo 8:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ngati mumtima mwanu munganene kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza chifukwa cha ntchito ya manja anga komanso mphamvu zanga,’+ 18 muzikumbukira kuti ndi Yehova Mulungu wanu amene amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbira kwa makolo anu, ngati mmene zilili lero.+
19 Koma mukadzaiwala Yehova Mulungu wanu nʼkutsatira milungu ina, kuitumikira ndiponso kuigwadira, ndikukuchenjezani lero kuti anthu inu mudzatha ndithu.+
-