1 Mafumu 17:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Eliya*+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi anauza Ahabu+ kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli amene ndimamʼtumikira, sikubwera mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”+ 2 Mafumu 17:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse ndiponso amasomphenya onse+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo muzisunga malamulo anga, mogwirizana ndi malamulo onse amene ndinalamula makolo anu ndiponso amene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.” Amosi 7:14, 15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri, koma ndinali mʼbusa+ ndiponso wosamalira* nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga kumene ndinkaweta nkhosa ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+
17 Eliya*+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi anauza Ahabu+ kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli amene ndimamʼtumikira, sikubwera mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”+
13 Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse ndiponso amasomphenya onse+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo muzisunga malamulo anga, mogwirizana ndi malamulo onse amene ndinalamula makolo anu ndiponso amene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.”
14 Amosi anayankha Amaziya kuti: “Ine sindinali mneneri kapena mwana wa mneneri, koma ndinali mʼbusa+ ndiponso wosamalira* nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga kumene ndinkaweta nkhosa ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisiraeli.’+