-
2 Mafumu 17:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Aisiraeli ankachita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo. Anapitiriza kumanga malo okwezeka mʼmizinda yawo yonse,+ kuyambira kunsanja ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.* 10 Iwo anapitiriza kuika zipilala zopatulika ndi mizati yopatulika*+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+
-