Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 17:9-11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Aisiraeli ankachita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo. Anapitiriza kumanga malo okwezeka mʼmizinda yawo yonse,+ kuyambira kunsanja ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.* 10 Iwo anapitiriza kuika zipilala zopatulika ndi mizati yopatulika*+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+ 11 Iwo anapitiriza kupereka nsembe zautsi pamalo okwezeka onse ngati mmene inkachitira mitundu imene Yehova anaithamangitsa mʼdzikolo chifukwa cha Aisiraeliwo.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa zokwiyitsa Yehova.

  • Ezekieli 23:4, 5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Wamkulu dzina lake anali Ohola,* wamngʼono anali Oholiba.* Akazi amenewa anakhala anga ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.

      5 Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Ankalakalaka kugona ndi amuna amene ankamukonda kwambiri+ omwe ndi Asuri amene ankakhala moyandikana naye.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena