-
2 Samueli 1:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Davide atamva zimenezi anagwira zovala zake nʼkuzingʼamba. Nawonso amuna onse amene anali naye anangʼamba zovala zawo. 12 Atatero, anayamba kulira ndi kusala kudya+ mpaka madzulo. Iwo ankalira maliro a Sauli, mwana wake Yonatani, anthu a Yehova ndiponso nyumba ya Isiraeli+ chifukwa anali ataphedwa ndi lupanga.
-