Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 62:8, 9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Yehova walumbira atakweza dzanja lake lamanja ndiponso mkono wake wamphamvu kuti:

      “Sindidzaperekanso mbewu zanu kwa adani anu kuti chikhale chakudya chawo,

      Ndipo alendo sadzamwa vinyo wanu watsopano amene munamupeza movutikira.+

       9 Koma anthu amene adzakolole mbewuzo ndi amene adzazidye ndipo adzatamanda Yehova.

      Amene adzakolole mphesa ndi amene adzamwe vinyoyo mʼmabwalo anga oyera.”+

  • Amosi 9:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Yehova wanena kuti, ‘Masiku adzafika,

      Pamene wolima adzapitirira wokolola,

      Ndipo woponda mphesa adzapitirira wonyamula mbewu.+

      Mʼmapiri akuluakulu mudzatuluka vinyo wotsekemera+

      Ndipo mʼmapiri angʼonoangʼono muzidzatuluka vinyo wambiri.+

  • Malaki 3:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Bweretsani gawo limodzi pa magawo 10 alionse* a zinthu zanu nʼkuziika mosungiramo zinthu zanga,+ kuti mʼnyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mageti akumwamba+ nʼkukukhuthulirani madalitso mpaka simudzasowa kanthu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena