-
Machitidwe 2:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: 17 ‘“Ndipo mʼmasiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzapereka* mzimu wanga kwa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi aakazi adzalosera. Anyamata adzaona masomphenya ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+ 18 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo ndipo iwo adzanenera.+
-