19 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndiponso zizindikiro padziko lapansi. Padzakhala magazi, moto ndi utsi wokwera mʼmwamba. 20 Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndiponso laulemerero la Yehova lisanafike.