21 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza kumwamba kuti mʼdziko lonse la Iguputo mugwe mdima wandiweyani.” 22 Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza kumwamba ndipo mʼdziko lonse la Iguputo munali mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+