-
Numeri 22:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Iye anatumiza anthu kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje* wamʼdziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane kuti: “Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja afika kuno. Iwo adzaza dziko lonse lapansi+ kumene munthu angayangʼane, ndipo akukhala pafupi penipeni ndi dziko langa. 6 Tsopano tabwerani chonde, mudzatemberere anthuwa+ chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo. Mwina ndingawagonjetse nʼkuwathamangitsa mʼdziko lino, chifukwa ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”
-