Deuteronomo 25:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Mʼthumba lanu musamakhale miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu,+ musamakhale ndi muyezo waukulu ndi wina waungʼono. Miyambo 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Yehova amanyasidwa ndi masikelo achinyengo,Koma sikelo imene imayeza molondola imamusangalatsa.*+ Hoseya 12:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Koma mʼmanja mwa wamalonda muli masikelo achinyengo.Iye amakonda kuba mwachinyengo.+
13 Mʼthumba lanu musamakhale miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu,+ musamakhale ndi muyezo waukulu ndi wina waungʼono.