-
2 Mafumu 16:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ahazi anayamba kulamulira ali ndi zaka 20 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+ 3 Anayenda mʼnjira ya mafumu a Isiraeli+ ndipo anafika mpaka potentha* pamoto mwana wake wamwamuna,+ potsatira zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu ina ankachita+ amene Yehova anawathamangitsa pamaso pa Aisiraeli.
-