15 Mzinda uwu unali wodzikuza ndipo unkakhala mosatekeseka.
Mumtima mwake unkanena kuti, ‘Ndine ndekha ndipo palibe wondiposa.’
Koma tsopano wakhala chinthu chodabwitsa,
Malo amene nyama zakutchire zimagonamo.
Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawu adzaimba mluzu ndipo adzapukusa mutu.”+