-
Yeremiya 27:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Tsopano ndapereka mayiko onsewa mʼmanja mwa mtumiki wanga, Mfumu Nebukadinezara+ ya ku Babulo. Ndamupatsanso ngakhale nyama zakutchire kuti zimutumikire. 7 Mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo, mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pa nthawi imeneyo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamupangitsa kuti akhale kapolo wawo.’+
-
-
Zekariya 2:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 “Bwera Ziyoni! Thawa iwe amene ukukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.*+ 8 Atapatsidwa ulemerero, Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene ankakulandani zinthu zanu,+ chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.+ 9 Ine ndidzawaloza mowaopseza, ndipo adzatengedwa ndi akapolo awo kuti akhale chuma cha akapolowo.’+ Mudzadziwa ndithu kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma.
-