-
Yeremiya 52:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9,+ njala inafika poipa kwambiri mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+ 7 Pamapeto pake, mpanda wa mzindawo unabooledwa ndipo asilikali onse anathawa mumzindawo usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo iwo anapitiriza kuthawa kulowera cha ku Araba.+
-