-
Yeremiya 52:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 10 la mweziwo, chomwe chinali chaka cha 19 cha Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+ 13 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu, nyumba iliyonse yaikulu komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu. 14 Kenako asilikali onse a Akasidi, omwe anali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, anagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+
-