37 Kenako Aisiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Panali amuna oyenda pansi pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+ 38 Ndipo gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ linapita limodzi ndi Aisiraeliwo. Linapitanso ndi nkhosa, mbuzi komanso ngʼombe zambirimbiri.