-
Ezekieli 34:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 “Nkhosa imene yasowa ndidzaifunafuna,+ imene yasochera ndidzaibweza. Imene yavulala ndidzaimanga povulalapo ndipo imene ili yofooka ndidzailimbitsa, koma yonenepa ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo kuti chikhale chakudya chake.”
17 Ponena za inu nkhosa zanga, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndatsala pangʼono kuweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake komanso pakati pa nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo.+
-