15 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza anthu ake.
Adani awo adzawaponyera miyala ndi gulaye, koma iwo adzawagonjetsa.+
Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.
Adzakhala ngati mbale zolowa zodzaza vinyo,
Ndiponso ngati magazi amene athiridwa mʼmakona a guwa lansembe.+