29 Ngakhale kuti munkawachenjeza kuti ayambenso kutsatira Chilamulo chanu, iwo ankadzikuza ndipo ankakana malamulo anu.+ Iwo anachimwa chifukwa sankatsatira ziweruzo zanu zimene munthu akamazitsatira amakhala ndi moyo.+ Anatseka makutu awo ndi kuumitsa makosi awo ndipo anakana kumvera.