Yobu 21:14, 15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Koma iwo amauza Mulungu woona kuti, ‘Tisiyeni! Sitikufuna kudziwa njira zanu.+ 15 Kodi Wamphamvuyonse ndi ndani kuti timutumikire?+ Ndipo kodi tingapindule chiyani ngati titamudziwa?’+ Salimo 73:13, 14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,Ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.+ 14 Ndinkavutika tsiku lonse,+Ndipo mʼmawa uliwonse ndinkadzudzulidwa.+ Yesaya 58:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 ‘Nʼchifukwa chiyani simukuona pamene tikusala kudya?+ Ndipo nʼchifukwa chiyani simukuona tikamadzisautsa?’+ Chifukwa chakuti pa tsiku lanu losala kudya mumachita zofuna zanu,*Ndipo mumapondereza antchito anu.+ Zefaniya 1:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mosamala kwambiri mu Yerusalemu,Ndipo ndidzaweruza anthu amene akukhala mosatekeseka* nʼkumaganiza kuti,‘Yehova sadzachita zabwino kapena zoipa.’+
14 Koma iwo amauza Mulungu woona kuti, ‘Tisiyeni! Sitikufuna kudziwa njira zanu.+ 15 Kodi Wamphamvuyonse ndi ndani kuti timutumikire?+ Ndipo kodi tingapindule chiyani ngati titamudziwa?’+
13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,Ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.+ 14 Ndinkavutika tsiku lonse,+Ndipo mʼmawa uliwonse ndinkadzudzulidwa.+
3 ‘Nʼchifukwa chiyani simukuona pamene tikusala kudya?+ Ndipo nʼchifukwa chiyani simukuona tikamadzisautsa?’+ Chifukwa chakuti pa tsiku lanu losala kudya mumachita zofuna zanu,*Ndipo mumapondereza antchito anu.+
12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mosamala kwambiri mu Yerusalemu,Ndipo ndidzaweruza anthu amene akukhala mosatekeseka* nʼkumaganiza kuti,‘Yehova sadzachita zabwino kapena zoipa.’+