-
Yesaya 61:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Wandituma kuti ndilengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,*
Ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu,+
Komanso kuti nditonthoze anthu onse amene akulira,+
3 Kuti ndisamalire anthu onse amene akulirira Ziyoni,
Kuti ndiwapatse nsalu yovala kumutu mʼmalo mwa phulusa,
Kuti ndiwapatse mafuta kuti azisangalala mʼmalo molira,
Kuti ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda mʼmalo mokhala otaya mtima.
-
-
Mateyu 11:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Bwerani kwa ine inu nonse amene mukugwira ntchito yotopetsa ndi olemedwa ndipo ndidzakutsitsimulani.
-