-
Luka 11:9-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Choncho ndikukuuzani, pitirizani kupempha+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.+ 10 Chifukwa aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira. 11 Kodi pakati panu pali bambo amene mwana wake atamupempha nsomba, angamupatse njoka mʼmalo mwa nsomba?+ 12 Kapenanso atamupempha dzira, kodi angamupatse chinkhanira? 13 Choncho ngati inuyo mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, ngakhale kuti ndinu oipa, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.”+
-