-
Luka 13:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mwininyumba akadzanyamuka nʼkukiya chitseko, inu mudzaima panja nʼkumagogoda chitsekocho, ndipo mudzanena kuti, ‘Ambuye titsegulireni.’+ Koma iye adzakuyankhani kuti: ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera.’ 26 Ndiyeno mudzayamba kunena kuti, ‘Tinkadya ndi kumwa pamaso panu ndipo inu munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.’+ 27 Koma iye adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera. Chokani pamaso panga, inu nonse ochita zinthu zosalungama!’
-