16 “Inu Yehova, Mulungu amene mumapereka moyo kwa anthu onse, sankhani munthu woti azitsogolera gululi. 17 Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse, kuti gulu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.”