-
Maliko 8:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Kenako iye anaitana gulu la anthu limodzi ndi ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira.+ 35 Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.+
-