4 Yesu anayambanso kuphunzitsa mʼmphepete mwa nyanja ndipo chigulu cha anthu chinasonkhana pafupi ndi iye. Choncho iye anakwera ngalawa nʼkukhala mʼngalawamo chapatali pangʼono ndi anthuwo, koma gulu lonse la anthulo linakhala mʼmphepete mwa nyanjayo.+