-
Maliko 4:30-32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Iye anapitiriza kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani kapena tingaufotokoze ndi fanizo lotani? 31 Uli ngati kanjere ka mpiru,* kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakangʼono kwambiri kuposa njere zonse zapadziko lapansi.+ 32 Koma akakafesa, kamamera nʼkukula kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo kamapanga nthambi zikuluzikulu, moti mbalame zamumlengalenga zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.”
-