22 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ mʼbale wake wapalamula mlandu wa kukhoti. Ndipo aliyense wonenera mʼbale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Komanso aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe chitsiru!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+
47 Ngati diso lako limakuchimwitsa,* ulitaye.+ Ndi bwino kuti ukalowe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi, kusiyana nʼkuti uponyedwe mu Gehena* uli ndi maso onse awiri,+