4 Mukasonkhana mʼdzina la Ambuye wathu Yesu, mudziwe kuti ndili nanu limodzi mumzimu komanso mumphamvu ya Ambuye wathu Yesu. 5 Choncho mupereke munthu ameneyu kwa Satana+ kuti thupilo liwonongedwe, nʼcholinga choti mzimuwo upulumutsidwe mʼtsiku la Ambuye.+