-
Maliko 12:24-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+ 25 Chifukwa akufa akadzaukitsidwa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 26 Koma pa mfundo yakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge mʼbuku la Mose munkhani yokhudza chitsamba chaminga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakoboʼ?+ 27 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+
-