-
Numeri 15:38, 39Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
38 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti azisokerera ulusi mʼmphepete mwa zovala zawo, ku mibadwo yawo yonse. Azisokereranso chingwe cha buluu pamwamba pa ulusi wa mphepete mwa zovalazo.+ 39 ‘Zovala zanu zizikhala ndi ulusi kuti mukaziona muzikumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwasunga.+ Musamatsatire zilakolako za mitima yanu ndi maso anu, chifukwa nʼzimene zikukupangitsani kuti musakhale okhulupirika kwa ine.*+
-