-
Luka 21:21-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri,+ ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali mʼmadera akumidzi asadzalowe mumzindawo, 22 chifukwa amenewa ndi masiku opereka chiweruzo* kuti zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe. 23 Tsoka kwa akazi oyembekezera komanso oyamwitsa ana mʼmasiku amenewo!+ Chifukwa mʼdzikoli mudzakhala mavuto aakulu komanso mkwiyo pa anthu awa.
-