-
Luka 19:24-26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Atatero anauza anthu amene anaima chapafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya minayo nʼkuipereka kwa amene ali ndi ndalama za mina 10.’+ 25 Koma iwo anamuuza kuti, ‘Mbuyathu, iyetu ali ndi ndalama za mina 10!’— 26 ‘Ndithu ndikukuuzani, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+
-