-
Luka 22:3-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Koma Satana analowa mwa Yudasi, amene ankadziwika kuti Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja.+ 4 Iye anapita kukakambirana ndi ansembe aakulu ndi oyangʼanira kachisi za mmene angamuperekere kwa iwo.+ 5 Iwo anasangalala ndipo anagwirizana kuti amupatse ndalama zasiliva.+ 6 Choncho iye anavomereza, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke kwa iwo popanda gulu la anthu pafupi.
-