-
Maliko 14:12-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ pamene mwamwambo ankapereka nsembe nyama ya Pasika,+ ophunzira ake anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako Pasika?”+ 13 Ndiyeno Yesu anatuma awiri mwa ophunzira akewo nʼkuwauza kuti: “Pitani mumzinda ndipo mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire,+ 14 ndipo mʼnyumba imene akalowe, mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 15 Iye akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukatikonzere Pasika mmenemo.” 16 Choncho ophunzirawo anapita nʼkulowa mumzinda ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo kumeneko anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
-
-
Luka 22:7-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Tsopano tsiku la Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa linafika, tsiku limene nsembe ya Pasika inkayenera kuperekedwa.+ 8 Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane nʼkuwauza kuti: “Pitani mukatikonzere Pasika kuti tidye.”+ 9 Iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti?” 10 Iye anawayankha kuti: “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire mʼnyumba imene akalowe.+ 11 Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 12 Ndiyeno munthu ameneyo akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.” 13 Choncho ananyamuka ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
-