-
Maliko 14:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Koma Petulo anayankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa nʼkukusiyani, ine ndekha sindidzathawa.”+ 30 Atatero Yesu anamuyankha kuti: “Ndithu ndikukuuza iwe kuti lero, usiku womwe uno, tambala asanalire kawiri, undikana katatu.”+ 31 Koma iye anapitiriza kunena kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ndipo ena onse anayamba kunenanso chimodzimodzi.+
-