-
Luka 21:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Komanso padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi.+ Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika chifukwa chothedwa nzeru poona kuti nyanja ikuchita mkokomo komanso kuwinduka. 26 Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha komanso chifukwa choyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, popeza mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.
-