17 Atadziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo nyumba yogawanika imagwa. 18 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana nayenso wagawanika, kodi ufumu wake ungakhalepo bwanji? Chifukwa inu mukunena kuti ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule.