-
Aroma 9:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Lonjezolo silinaperekedwe pa nthawi iyi yokha. Linaperekedwanso pamene Rabeka ankayembekezera kubereka ana amapasa a Isaki kholo lathu lija.+ 11 Mapasawo asanabadwe ndiponso asanachite chabwino kapena choipa chilichonse, Mulungu anasonyeza kuti cholinga chake chidzadalira iye amene amaitana, osati zochita za munthu. 12 Choncho anauza Rabeka kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamngʼono.”+
-