46 Ndiye mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzalandira mphoto yotani?+ Kodi okhometsa msonkho sachitanso zomwezo? 47 Ngati mukupereka moni kwa abale anu okha, kodi nʼchiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo?