Ekisodo 22:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Mukabwereketsa ndalama kwa munthu aliyense wosauka* pakati pa anthu anga, kwa munthu amene ali pafupi ndi inu, musakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira kwa iye. Musamuuze kuti apereke chiwongoladzanja.+ Levitiko 25:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Mukamukongoza ndalama musamafunepo chiwongoladzanja+ kapena kumupatsa chakudya kuti mupezerepo phindu. Deuteronomo 23:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Mlendo mungamulipiritse chiwongoladzanja,+ koma mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+ Salimo 37:25, 26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+ 26 Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.
25 Mukabwereketsa ndalama kwa munthu aliyense wosauka* pakati pa anthu anga, kwa munthu amene ali pafupi ndi inu, musakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira kwa iye. Musamuuze kuti apereke chiwongoladzanja.+
37 Mukamukongoza ndalama musamafunepo chiwongoladzanja+ kapena kumupatsa chakudya kuti mupezerepo phindu.
20 Mlendo mungamulipiritse chiwongoladzanja,+ koma mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+
25 Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+ 26 Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.