16 Mofanana ndi zimenezi, mbewu zimene zafesedwa pamiyala ndi mawu amene afesedwa mwa anthu omwe amati akangomva mawuwo, amawalandira mosangalala.+ 17 Koma iwo amakhala opanda mizu ndipo amapitirizabe kwakanthawi. Ndiyeno akangoyamba kuvutitsidwa kapena kuzunzidwa chifukwa cha mawuwo, amapunthwa.