Mateyu 8:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Yesu ataona kuti gulu la anthu lamuzungulira, analamula kuti achoke nʼkupita kutsidya lina.+ Mateyu 8:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndiyeno atakwera mʼngalawa, ophunzira ake anamʼtsatira.+ Maliko 4:35, 36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”+ 36 Choncho atauza gulu la anthulo kuti lizipita, ophunzirawo anachoka naye pangalawa imene anakwera ija, koma analinso ndi ngalawa zina.+
35 Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”+ 36 Choncho atauza gulu la anthulo kuti lizipita, ophunzirawo anachoka naye pangalawa imene anakwera ija, koma analinso ndi ngalawa zina.+