-
Luka 7:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Atayandikira pageti la mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro. Munthu amene anamwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo kwa mayi ake.+ Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye. Gulu lalikulu ndithu la anthu ochokera mumzindawo linali limodzi ndi mayiwo. 13 Ambuye ataona mayiwo anawamvera chisoni,+ ndipo anawauza kuti: “Tontholani mayi.”+
-