-
Maliko 6:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndiyeno Mfumu Herode inamva zimenezi chifukwa dzina la Yesu linatchuka kwambiri ndipo anthu ankanena kuti: “Yohane Mʼbatizi wauka kwa akufa nʼchifukwa chake akuchita ntchito zamphamvu.”+ 15 Koma ena ankanena kuti: “Ndi Eliya.” Ndipo ena ankanena kuti: “Ndi mneneri ngati mmene analili aneneri akale.”+ 16 Koma Herode atamva za Yesu ananena kuti: “Ndithu Yohane amene ndinamudula mutu uja waukitsidwadi.”
-